8 Mukapereka nsembe nyama yakhungu, mumanena kuti: “Palibe cholakwika.” Mukapereka nsembe nyama yolumala kapena yodwala, mumati: “Palibe vuto.”’”+
“Pitani nazo kwa bwanamkubwa wanu. Kodi akakondwera nanu? Kapena kodi akakulandirani bwino?” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.