-
Ezekieli 8:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ndipo akuluakulu 70 a nyumba ya Isiraeli anali ataimirira patsogolo pa mafanowo. Pakati pawo panalinso Yaazaniya mwana wa Safani.+ Aliyense ananyamula chiwaya chofukizira nsembe mʼmanja mwake ndipo utsi wonunkhira wa zofukizazo unkakwera mʼmwamba.+ 12 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Isiraeli akuchita mumdima? Kodi waona zimene aliyense wa iwo akuchita mʼzipinda zake zamkati mmene muli mafano ake? Iwo akunena kuti, ‘Yehova sakutiona. Yehova wachokamo mʼdziko muno.’”+
-