-
Mika 3:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Koma mumadana ndi zinthu zabwino+ ndipo mumakonda zinthu zoipa.+
Mumasenda khungu la anthu anga nʼkuchotsa mnofu pamafupa awo.+
3 Mumadyanso mnofu wa anthu anga,+
Ndipo mumasenda khungu lawo.
Mumaswa mafupa awo nʼkuwaphwanyaphwanya.+
Ngati zinthu zimene zaphikidwa mumphika* komanso ngati nyama imene ili mumphika.
4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize,
Koma sadzawayankha.
-