-
2 Mafumu 17:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Atayamba kukhala kumeneko, sankaopa* Yehova. Choncho Yehova anawatumizira mikango+ ndipo inapha ena mwa anthuwo. 26 Mfumu ya Asuri inauzidwa kuti: “Mitundu imene munaichotsa kwawo nʼkukaiika mʼmizinda ya ku Samariya sikudziwa chipembedzo* cha Mulungu wa kumeneko. Choncho iye wakhala akuwatumizira mikango imene ikuwapha chifukwa palibe amene akudziwa chipembedzo cha Mulungu wa kumeneko.”
-