-
2 Mafumu 16:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kenako Mfumu Ahazi anapita kukakumana ndi Tigilati-pilesere mfumu ya Asuri ku Damasiko. Kumeneko anaonako guwa lansembe, choncho Mfumu Ahazi anatumizira wansembe Uliya pulani ya guwalo.+ 11 Wansembe Uliya+ anamanga guwalo+ mogwirizana ndi malangizo onse amene Mfumu Ahazi anamutumizira ali ku Damasiko. Wansembe Uliya anamaliza kumanga guwalo Mfumu Ahazi asanabwere kuchokera ku Damasiko.
-
-
Yeremiya 5:31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+
Koma kodi mudzachita chiyani mapeto akadzafika?”
-