4 “Aliyense asamale ndi mnzake,
Ndipo musamakhulupirire ngakhale mʼbale wanu.
Chifukwa munthu aliyense ndi wachinyengo,+
Ndipo munthu aliyense akunenera mnzake zoipa.+
5 Aliyense amapusitsa mnzake,
Ndipo palibe amene amalankhula zoona.
Aphunzitsa lilime lawo kulankhula chinyengo.+
Iwo amadzitopetsa okha pochita zinthu zoipa.