-
2 Mafumu 20:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Mʼmasiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pangʼono kufa.+ Ndiyeno mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita, chifukwa iweyo ufa ndithu, suchira.’”+ 2 Hezekiya atamva zimenezi, anatembenukira kukhoma nʼkuyamba kupemphera kwa Yehova kuti: 3 “Yehova, chonde ndikukupemphani kuti mukumbukire kuti ndinayenda pamaso panu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wonse komanso ndachita zabwino pamaso panu.”+ Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.
-