-
2 Mafumu 20:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Pamene Yesaya ankabwerera, asanafike nʼkomwe pabwalo lapakati, Yehova anamuuza kuti:+ 5 “Bwerera, ukauze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako wanena kuti: “Ndamva pemphero lako ndipo ndaona misozi yako.+ Ndikuchiritsa.+ Pa tsiku lachitatu udzapita kunyumba ya Yehova.+ 6 Ndiwonjezera zaka 15 pa moyo* wako ndipo ndidzapulumutsa iweyo ndi mzindawu mʼmanja mwa mfumu ya Asuri.+ Ndidzateteza mzindawu chifukwa cha ineyo ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.”’”+
-