-
2 Mafumu 20:8-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Hezekiya anali atafunsa Yesaya kuti: “Kodi chizindikiro+ chakuti Yehova andichiritsa ndipo ndidzapitadi kunyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu nʼchiyani?” 9 Yesaya anayankha kuti: “Chizindikiro chochokera kwa Yehova chosonyeza kuti Yehova adzakwaniritsadi mawu ake, ndi ichi: Kodi ukufuna kuti mthunzi uyende masitepe* 10 kupita kutsogolo, kapena uyende masitepe 10 kubwerera mʼmbuyo?”+ 10 Hezekiya anayankha kuti: “Nʼzosavuta kuti mthunzi upite kutsogolo masitepe 10, koma nʼzovuta kuti ubwerere mʼmbuyo masitepe 10.” 11 Choncho mneneri Yesaya anafuulira Yehova ndipo iye anachititsa mthunzi umene unali utapita kale kutsogolo kuti ubwerere mʼmbuyo pamasitepe a Ahazi. Mthunziwo unabwerera mʼmbuyo masitepe 10.+
-