Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 18:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndapalana ubwenzi ndi Abulahamu kuti aphunzitse ana ake ndi mbadwa zake zonse* kuyenda mʼnjira ya Yehova. Azichita zimenezi pochita zabwino ndi zachilungamo+ kuti Yehova adzakwaniritse zimene ananena zokhudza Abulahamu.”

  • Deuteronomo 4:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma samalani ndipo mukhale tcheru* kuti musaiwale zinthu zimene maso anu anaona, komanso kuti zinthu zimenezo zisachoke mumtima mwanu masiku onse a moyo wanu. Ana anu ndi zidzukulu zanu muziwauzanso zinthu zimenezo.+

  • Yoswa 4:21-24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Kenako anauza Aisiraeli kuti: “Mʼtsogolomu ana anu akamadzafunsa abambo awo kuti, ‘Kodi miyalayi ndi ya chiyani?’+ 22 Muzidzauza anawo kuti, ‘Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano panthaka youma.+ 23 Izi zinachitika pamene Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano, mpaka iwo atawoloka. Zinachitika mofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anachita pa Nyanja Yofiira, pamene anaphwetsa madzi a nyanjayo, mpaka onse atawoloka.+ 24 Yehova anachita zimenezi kuti anthu onse apadziko lapansi adziwe kuti dzanja lake ndi lamphamvu,+ ndiponso kuti inu muziopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse.’”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena