-
2 Mafumu 20:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Kenako mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya nʼkuifunsa kuti: “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, nanga anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.”+ 15 Atatero Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani mʼnyumba mwanu?” Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili mʼnyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.”
-