Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 24:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo atumiki ake atauzungulira.

  • 2 Mafumu 24:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha mʼnyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapanga kuti zikhale za mʼkachisi wa Yehova.+ Zimenezi zinachitika mogwirizana ndi zimene Yehova analosera.

  • 2 Mafumu 25:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Akasidi anaphwanyaphwanya zipilala zakopa+ zomwe zinali mʼnyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndiponso thanki ya kopa yosungira madzi+ zimene zinali mʼnyumba ya Yehova, nʼkutenga kopa wake kupita naye ku Babulo.+

  • 2 Mbiri 36:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse, zazikulu ndi zazingʼono, zamʼnyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma cha mʼnyumba ya Yehova, chuma cha mfumu ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse nʼkupita nacho ku Babulo.+

  • Danieli 1:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 Mʼchaka chachitatu cha ufumu wa Mfumu Yehoyakimu+ ya Yuda, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inabwera ku Yerusalemu ndipo inazungulira mzindawo.+ 2 Kenako Yehova anapereka Mfumu Yehoyakimu ya Yuda mʼmanja mwake,+ limodzi ndi zina mwa ziwiya za mʼnyumba ya* Mulungu woona. Nebukadinezara anatenga ziwiyazo nʼkupita nazo kudziko la Sinara,*+ kunyumba* ya mulungu wake ndipo anakaziika mʼnyumba yosungiramo chuma ya mulungu wake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena