-
Yeremiya 32:28, 29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Tsopano ndikupereka mzindawu mʼmanja mwa Akasidi ndi mʼmanja mwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo, ndipo aulanda.+ 29 Akasidi amene akumenyana ndi anthu amumzindawu adzabwera nʼkuyatsa mzindawu moti udzapseratu.+ Adzawotchanso nyumba zimene pamadenga ake anthu ankaperekerapo nsembe kwa Baala komanso nsembe zachakumwa kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.’+
-