6 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo+ nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo ndipo anaipatsa chigamulo. 7 Iwo anapha ana aamuna a Zedekiya iye akuona, kenako Zedekiyayo anamʼchititsa khungu. Atatero anamumanga ndi maunyolo akopa nʼkupita naye ku Babulo.+