-
Levitiko 25:39-42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Mʼbale wanu amene mukukhala naye pafupi akasauka nʼkudzigulitsa kwa inu,+ musamamugwiritse ntchito ngati kapolo.+ 40 Muzimuona ngati waganyu+ komanso ngati mlendo. Azikugwirirani ntchito mpaka Chaka cha Ufulu. 41 Mʼchaka chimenecho iye ndi ana ake* azichoka nʼkubwerera kwa achibale ake. Azibwerera kumalo a makolo ake.+ 42 Aisiraeli ndi akapolo anga amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ Choncho asamadzigulitse ngati mmene anthu amagulitsira kapolo.
-