-
Yeremiya 15:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ndiyeno akakufunsa kuti, ‘Tipite kuti?’ uwayankhe kuti, ‘Yehova wanena kuti:
“Amene akuyenera kufa ndi mliri afe ndi mliri!
Amene akuyenera kufa ndi lupanga afe ndi lupanga!+
Amene akuyenera kufa ndi njala yaikulu afe ndi njala yaikulu!
Amene akuyenera kutengedwa kupita ku ukapolo atengedwe kupita ku ukapolo!”’+
-
-
Yeremiya 29:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 ‘Ndidzawathamangitsa ndi lupanga,+ njala ndi mliri ndipo ndidzawapangitsa kuti akhale chinthu chochititsa mantha kwa maufumu onse apadziko lapansi.+ Komanso ndidzawachititsa kuti akhale chinthu chotembereredwa, chodabwitsa, chochiimbira mluzu+ ndiponso kuchinyoza pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene ndidzawabalalitsireko.+
-