Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 25:4-7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno mpanda wa mzindawo unabooledwa+ ndipo asilikali onse anathawa usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo mfumu inayamba kuthawa kulowera cha ku Araba.+ 5 Koma asilikali a Akasidi anayamba kuthamangitsa mfumuyo ndipo anaipeza mʼchipululu cha Yeriko. Zitatero asilikali onse a mfumuyo anabalalika nʼkuisiya yokha. 6 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo+ nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo ndipo anaipatsa chigamulo. 7 Iwo anapha ana aamuna a Zedekiya iye akuona, kenako Zedekiyayo anamʼchititsa khungu. Atatero anamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo.+

  • Yeremiya 52:7-11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Pamapeto pake, mpanda wa mzindawo unabooledwa ndipo asilikali onse anathawa mumzindawo usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo iwo anapitiriza kuthawa kulowera cha ku Araba.+ 8 Koma asilikali a Akasidi anayamba kuthamangitsa Zedekiya+ ndipo anamupeza mʼchipululu cha Yeriko. Zitatero asilikali onse a mfumuyo anabalalika nʼkuisiya yokha. 9 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo mʼdziko la Hamati ndipo anaipatsa chigamulo. 10 Ndipo mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya, iye akuona. Inaphanso akalonga onse a ku Yuda ku Ribila komweko. 11 Kenako mfumu ya Babulo inachititsa khungu Zedekiya,+ inamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo ndipo inamuika mʼndende mpaka tsiku la imfa yake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena