8 Yehoyakini+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 18 ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Nehusita mwana wa Elinatani. 9 Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene bambo ake anachita.