12 Kenako ndinapereka makalata a pangano ogulira mundawo kwa Baruki+ mwana wa Neriya,+ mwana wa Maseya. Ndinapereka makalatawo pamaso pa Hanameli mwana wa mʼbale wawo wa bambo anga, pamaso pa mboni zimene zinasaina makalatawo ndi pamaso pa Ayuda onse amene anali mʼBwalo la Alonda.+