36 Yehoyakimu+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 25 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Ruma ndipo dzina lawo linali Zebida mwana wa Pedaya.
25Awa ndi mawu amene Yeremiya anauzidwa onena za anthu onse a mu Yuda mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, chimenenso chinali chaka choyamba cha ulamuliro wa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo.