43 Tsopano izi ndi zimene Yehova wanena,
Mlengi wako iwe Yakobo, amene anakupanga iwe Isiraeli.+ Iye wanena kuti:
“Usachite mantha, chifukwa ine ndakuwombola.+
Ndakuitana pokutchula dzina lako.
Iwe ndiwe wanga.
2 Ukamadzadutsa pamadzi, ine ndidzakhala nawe.+
Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakukokolola.+
Ukamadzayenda pamoto sudzapsa
Ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.