35 Anthu amene akukhala mu Ziyoni akunena kuti, ‘Chiwawa chimene anachitira ine ndi thupi langa chigwerenso Babulo.’+
Ndipo Yerusalemu akunena kuti, ‘Magazi anga akhale pa anthu amene akukhala mʼdziko la Kasidi.’”
36 Choncho Yehova wanena kuti:
“Ine ndikuteteza pa mlandu wako,+
Ndipo ndidzakubwezerera adani ako.+
Ndidzaphwetsa nyanja yake ndi zitsime zake.+