-
Yeremiya 51:41Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Babulo wakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa mitundu ya anthu.
-
-
Chivumbulutso 18:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Amalonda amene ankagulitsa zinthu zimenezi, amene analemera chifukwa cha iye, adzaima patali chifukwa cha mantha poona mmene akuzunzikira ndipo adzamulirira ndi kumva chisoni. 16 Iwo azidzati: ‘Zomvetsa chisoni! Zomvetsa chisoni! Iwe mzinda waukulu, umene unkavala zovala zapamwamba, zapepo ndi zofiira kwambiri. Iwe mzinda umene unakongoletsedwa mochititsa chidwi ndi zodzikongoletsera zagolide, mwala wamtengo wapatali ndi ngale.+
-