-
2 Mbiri 28:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Patapita nthawi, Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri anabwera kwa iye ndipo anangomuwonjezera mavuto+ mʼmalo momulimbikitsa. 21 Ahazi anali atatenga zinthu za mʼnyumba ya Yehova, za mʼnyumba ya mfumu+ ndi zamʼnyumba za akalonga nʼkuzipereka ngati mphatso kwa mfumu ya Asuri, koma zimenezi sizinamuthandize. 22 Ndipo pa nthawi imene Mfumu Ahazi ankakumana ndi mavuto, anawonjezera kuchita zosakhulupirika kwa Yehova.
-