Levitiko 18:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Musamachite zinthu zimene anthu a ku Iguputo kumene munkakhala amachita, komanso musamachite zinthu zimene anthu amʼdziko la Kanani limene ndikukupititsani amachita.+ Ndipo musamakatsatire malamulo awo. Levitiko 18:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Choncho muzisunga malamulo anga popewa kuchita miyambo yonyansa iliyonse imene anthu akhala akuchita inu musanafike,+ kuti musadzidetse ndi miyamboyo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’” Levitiko 20:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Musamatsatire malamulo a mitundu imene ndikuithamangitsa pamaso panu,+ chifukwa iwo amachita zonsezi ndipo amandinyansa.+ Deuteronomo 12:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 mukasamale kuti musakagwidwe mumsampha wawo, pambuyo poti awonongedwa ndi kuchotsedwa pamaso panu. Musakafunse zokhudza milungu yawo kuti, ‘Kodi mitundu imeneyi inkatumikira bwanji milungu yawo? Inenso ndichita zomwezo.’+
3 Musamachite zinthu zimene anthu a ku Iguputo kumene munkakhala amachita, komanso musamachite zinthu zimene anthu amʼdziko la Kanani limene ndikukupititsani amachita.+ Ndipo musamakatsatire malamulo awo.
30 Choncho muzisunga malamulo anga popewa kuchita miyambo yonyansa iliyonse imene anthu akhala akuchita inu musanafike,+ kuti musadzidetse ndi miyamboyo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
23 Musamatsatire malamulo a mitundu imene ndikuithamangitsa pamaso panu,+ chifukwa iwo amachita zonsezi ndipo amandinyansa.+
30 mukasamale kuti musakagwidwe mumsampha wawo, pambuyo poti awonongedwa ndi kuchotsedwa pamaso panu. Musakafunse zokhudza milungu yawo kuti, ‘Kodi mitundu imeneyi inkatumikira bwanji milungu yawo? Inenso ndichita zomwezo.’+