-
Yeremiya 8:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 “Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “mafupa a mafumu a Yuda, a akalonga awo, a ansembe, a aneneri ndi a anthu okhala mu Yerusalemu adzatulutsidwa mʼmanda awo. 2 Mafupawo adzamwazidwa padzuwa, pamwezi ndi panyenyezi zonse zakumwamba* zimene ankazikonda, kuzitumikira, kuzitsatira, kuzifunafuna ndi kuzigwadira.+ Anthu sadzasonkhanitsa mafupawo pamodzi nʼkuwaika mʼmanda ndipo adzakhala ngati manyowa panthaka.”+
-
-
Zefaniya 1:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 “Ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwononga Yuda,
Ndiponso anthu onse okhala mu Yerusalemu.
Ndidzawononga chilichonse chokhudza Baala+ pamalowa.
Ndidzawononganso ansembe komanso dzina la ansembe a mulungu wachilendo.+
5 Ndidzawononga anthu amene amakwera padenga nʼkumagwadira magulu a zinthu zakumwamba.*+
Komanso amene amagwada ndiponso kulumbira kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+
Koma nʼkumalumbiranso kuti adzakhala okhulupirika kwa Malikamu.+
-