-
Yeremiya 16:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 ‘Komabe masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene sadzalumbiranso kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa Aisiraeli mʼdziko la Iguputo!”+ 15 Koma adzalumbira kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa Aisiraeli mʼdziko lakumpoto komanso kuchokera mʼmayiko onse kumene anawabalalitsira!” Ineyo ndidzawabwezera kudziko lawo limene ndinapatsa makolo awo.’+
-