-
Yeremiya 3:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Nditaona zimenezo, ndinathamangitsa Isiraeli wosakhulupirikayo ndipo ndinamupatsa kalata yotsimikizira kuti ukwati watha+ chifukwa anachita chigololo.+ Koma Yuda mchemwali wake, amene ndi wachinyengo, sanachite mantha. Nayenso anayamba kuchita uhule.+ 9 Iye ankaona kuti kuchita uhulewo si vuto moti anapitiriza kuipitsa dzikolo ndipo ankachita chigololo ndi miyala komanso mitengo.+
-