-
Ezekieli 8:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Choncho ndinalowa ndipo nditayangʼana ndinaona zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwawa, nyama zonyansa+ komanso mafano onse onyansa* a Aisiraeli.+ Zithunzizo zinajambulidwa pamakoma onse mochita kugoba. 11 Ndipo akuluakulu 70 a nyumba ya Isiraeli anali ataimirira patsogolo pa mafanowo. Pakati pawo panalinso Yaazaniya mwana wa Safani.+ Aliyense ananyamula chiwaya chofukizira nsembe mʼmanja mwake ndipo utsi wonunkhira wa zofukizazo unkakwera mʼmwamba.+
-