8 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Musalole kuti aneneri anu komanso anthu ochita zamaula amene ali pakati panu akupusitseni+ ndipo musamvere maloto amene alota. 9 Chifukwa ‘akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa. Ine sindinawatume,’+ akutero Yehova.”’”