3 Iye anamanganso malo okwezeka amene Hezekiya bambo ake anachotsa.+ Komanso anamanga maguwa ansembe a Baala ndi mzati wopatulika,+ ngati mmene Ahabu mfumu ya Isiraeli anachitira.+ Manase ankalambira ndiponso kutumikira gulu lonse la zinthu zakuthambo.+