-
Deuteronomo 13:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Koma mneneri kapena woloserayo muzimupha,+ chifukwa akulimbikitsa anthu kuti azipandukira Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo komanso kukuwombolani mʼnyumba yaukapolo. Munthu ameneyo akufuna akupatutseni panjira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muziyendamo. Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+
-
-
Yeremiya 29:32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Yehova wanena kuti, ‘Ine ndilanga Semaya wa ku Nehelamu ndi mbadwa zake. Sipadzapezeka mwamuna aliyense wochokera mʼbanja lake amene adzapulumuke pakati pa anthu awa. Ndipo iye sadzaona zabwino zimene ndidzachitire anthu anga chifukwa walimbikitsa anthu kuti apandukire Yehova,’ akutero Yehova.”’”
-