-
Yeremiya 44:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ine ndigwira anthu amene anatsala ku Yuda omwe anatsimikiza mtima kuti apite mʼdziko la Iguputo nʼkumakakhala kumeneko, moti onsewo adzafera mʼdziko la Iguputo.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga komanso adzafa ndi njala. Kuyambira munthu wamba ndi wolemekezeka yemwe, onse adzaphedwa ndi lupanga komanso adzafa ndi njala. Iwo adzakhala otembereredwa, chinthu chochititsa mantha, chinthu chonyozeka ndi chochititsa manyazi.+
-
-
Ezekieli 17:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Gulu lalikulu la asilikali komanso asilikali ambirimbiri a Farao sadzamuthandiza pankhondo,+ adani akadzamanga malo okwera omenyerapo nkhondo ndiponso mpanda womenyerapo nkhondo nʼcholinga chakuti aphe anthu ambiri. 18 Iye wanyoza lumbiro limenelo komanso waphwanya pangano. Ngakhale kuti analonjeza,* iye wachita zinthu zonsezi ndipo sadzapulumuka.”’
-