Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 51:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Chifukwa Yehova adzatonthoza Ziyoni.+

      Iye adzatonthoza malo ake onse amene anawonongedwa.+

      Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni+

      Ndipo dera lake lachipululu lidzakhala ngati munda wa Yehova.+

      Mwa iye mudzakhala kusangalala ndi kukondwera,

      Kuyamikira ndi kuimba nyimbo zosangalatsa.+

  • Yeremiya 30:18, 19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova wanena kuti:

      “Ndikusonkhanitsa anthu amʼmatenti a Yakobo amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,+

      Ndipo ndidzamvera chisoni malo okhala a Yakobo.

      Mzinda udzamangidwanso pamalo amene unali poyamba,+

      Ndipo nsanja yokhala ndi mpanda wolimba idzakhala pamalo ake oyenerera.

      19 Kwa iwo kudzamveka mawu oyamikira ndi phokoso la kuseka kwa anthu.+

      Ndidzawachulukitsa moti sadzakhala ochepa.+

      Ndidzawachititsa kuti akhale ambiri,*

      Ndipo sadzakhala anthu ochepa.+

  • Amosi 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anatengedwa kupita ku ukapolo.+

      Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja nʼkumakhalamo.+

      Adzalima minda ya mpesa nʼkumwa vinyo wake.+

      Adzalimanso minda nʼkudya zipatso zake.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena