25 Anthu amenewa adzakhala mʼdziko limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu ankakhala.+ Iwo adzakhala mʼdzikomo ndi ana awo komanso zidzukulu zawo+ mpaka kalekale.+ Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wawo mpaka kalekale.+