23 Aamoni ndi Amowabu anaukira anthu okhala kudera lamapiri la Seiri+ ndipo anayamba kuwapha mpaka kuwamaliza. Atatha kupha anthu a ku Seiri, iwo anaphana okhaokha.+
22 Ndidzagonjetsa maufumu ndi kuchotsa mphamvu za maufumu a anthu a mitundu ina.+ Ndidzawononga magaleta* ndi okwera pamagaletawo. Mahatchi* ndi okwera pamahatchiwo adzaphedwa ndipo aliyense adzaphedwa ndi mʼbale wake ndi lupanga.’”+