-
2 Mafumu 24:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Choncho iye anatenga Yehoyakini+ nʼkupita naye ku Babulo.+ Ku Yerusalemu anatenganso mayi a mfumuyo, akazi ake, nduna za panyumba yake komanso akuluakulu a mʼdzikolo, nʼkupita nawo ku Babulo. 16 Mfumu ya Babulo inatenganso asilikali onse amphamvu okwana 7,000, amisiri okwana 1,000 komanso anthu osula zitsulo* ndipo onse anali amuna amphamvu komanso ophunzitsidwa kumenya nkhondo nʼkupita nawo ku Babulo.
-