-
Ezekieli 40:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kumbali iliyonse ya geti lakumʼmawa kunali zipinda zitatu za alonda. Zipinda zitatuzo zinali zazikulu mofanana, ndipo zipilala zamʼmbali zimene zinali mbali iliyonse zinalinso zofanana.
-
-
Ezekieli 46:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
46 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Kanyumba kapageti la bwalo lamkati kamene kayangʼana kumʼmawa+ kazikhala kotseka+ kwa masiku 6 ogwira ntchito.+ Koma pa tsiku la Sabata ndi pa tsiku limene mwezi watsopano waoneka kazitsegulidwa. 2 Mtsogoleri azilowa kuchokera panja kudzera pakhonde la kanyumba kapagetiko+ ndipo aziima pafupi ndi felemu lagetilo. Ndiyeno ansembe azimuperekera nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zake zamgwirizano. Mtsogoleriyo azigwada nʼkuwerama pakhomo la kanyumba kapageti kenako nʼkutuluka. Koma getilo lisamatsekedwe mpaka madzulo.
-