-
2 Mbiri 13:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Koma ife, Mulungu wathu ndi Yehova+ ndipo sitinamusiye. Ansembe athu, omwe ndi mbadwa za Aroni, akutumikira Yehova, ndipo Alevi akuthandiza pa ntchitoyi. 11 Iwo akupereka nsembe zopsereza kwa Yehova mʼmawa uliwonse+ ndi madzulo alionse limodzi ndi mafuta onunkhira.+ Ndipo mikate yosanjikiza*+ ili patebulo la golide woyenga bwino. Komanso madzulo alionse+ amayatsa nyale zomwe zili pachoikapo nyale chagolide.+ Tikuchita zimenezi chifukwa tikukwaniritsa udindo wathu kwa Yehova Mulungu wathu, koma inuyo mwamusiya.
-