-
Numeri 16:39, 40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Choncho wansembe Eleazara anatenga zofukizira zakopa zimene anthu amene anapsa ndi moto aja anabweretsa, ndipo anazisula nʼkupanga timalata tokutira guwa lansembe, 40 mogwirizana ndi zimene Yehova anamuuza kudzera mwa Mose. Timalatato tinali chikumbutso kwa Aisiraeli kuti munthu wamba* amene si mbadwa ya Aroni asayandikire kwa Yehova kuti akapereke nsembe zofukiza.+ Anachita zimenezi kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi anthu amene ankamutsatira anachita.+
-
-
Ezekieli 44:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ana a Zadoki, omwe ndi Alevi ansembe,+ amene ankagwira ntchito zapamalo anga opatulika pa nthawi imene Aisiraeli anachoka kwa ine,+ ndi amene adzandiyandikire nʼkumanditumikira. Iwo adzaima pamaso panga nʼkundipatsa mafuta+ ndi magazi,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 16 ‘Iwo ndi amene adzalowe mʼmalo anga opatulika. Adzayandikira tebulo langa kuti anditumikire+ ndipo adzagwira ntchito zimene apatsidwa ponditumikira.+
-