15 Makoma a mkati mwa nyumbayo anawamanga ndi matabwa akuluakulu a mkungudza. Mkati mwa nyumbayo, kuchokera pansi mpaka kudenga anakutamo ndi matabwa. Komanso pansi pa nyumbayo anaikapo matabwa akuluakulu a mitengo ya junipa.*+
5 Nyumba yaikuluyo anaikuta ndi matabwa a mitengo ya junipa,* kenako anaikutanso ndi golide wabwino.+ Atatero, anaikongoletsa ndi matcheni+ ndiponso zithunzi za mitengo yakanjedza zojambula mochita kugoba.+