10 Ndipo mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya, iye akuona. Inaphanso akalonga onse a ku Yuda ku Ribila komweko. 11 Kenako mfumu ya Babulo inachititsa khungu Zedekiya,+ inamumanga ndi maunyolo akopa nʼkupita naye ku Babulo ndipo inamuika mʼndende mpaka tsiku la imfa yake.