-
1 Mafumu 22:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Kenako mngelo*+ wina anabwera kudzaima pamaso pa Yehova nʼkunena kuti, ‘Ine ndikamʼpusitsa.’ Yehova anamufunsa kuti, ‘Ukamʼpusitsa bwanji?’ 22 Iye anayankha kuti, ‘Ndipita kukakhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse.’+ Ndiyeno Mulungu anati, ‘Ukamʼpusitsadi ndipo zikakuyendera bwino. Pita ukachite zimenezo.’
-
-
2 Atesalonika 2:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 komanso akugwiritsa ntchito njira iliyonse yachinyengo+ kuti apusitse amene akupita kukawonongedwa. Izi zidzakhala chilango kwa iwo chifukwa sanalandire komanso kukonda choonadi kuti adzapulumuke. 11 Nʼchifukwa chake Mulungu walola kuti iwo apusitsidwe ndi ziphunzitso zabodza nʼcholinga choti azikhulupirira bodza,+
-