-
Ekisodo 6:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Choncho ndidzakutengani kuti mukhale anthu anga, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.+ Inuyo mudzadziwadi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndikukupulumutsani ku ntchito yokakamiza imene Aiguputo akukugwiritsani. 8 Ine ndidzakulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira* kuti ndidzalipereka kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale lanu.+ Ine ndine Yehova.’”+
-