16 (Pakuti inu mukudziwa bwino mmene tinkakhalira mʼdziko la Iguputo komanso mmene tinadutsira pakati pa anthu a mitundu ina pa ulendo wathuwu.+ 17 Inu munkaona zinthu zawo zonyansa ndi mafano awo onyansa+ amtengo ndi amwala, asiliva ndi agolide amene anali pakati pawo.)