-
Ekisodo 13:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Farao atalola kuti Aisiraeli apite, Mulungu sanawadutsitse mʼdziko la Afilisiti ngakhale kuti inali njira yaifupi, chifukwa Mulungu anati: “Anthu angasinthe maganizo akakumana ndi nkhondo ndipo angabwerere ku Iguputo.” 18 Choncho Mulungu anachititsa kuti Aisiraeli adutse njira yaitali yodzera mʼchipululu chapafupi ndi Nyanja Yofiira.+ Koma potuluka mʼdziko la Iguputo, Aisiraeli anayenda mwadongosolo ngati magulu a asilikali.
-
-
Ekisodo 15:22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Kenako Mose anatsogolera Isiraeli kuchoka ku Nyanja Yofiira ndipo analowa mʼchipululu cha Shura. Iwo anayenda mʼchipululumo kwa masiku atatu, koma sanapeze madzi.
-