13 “Uuze Aisiraeli kuti, ‘Muonetsetse kuti mukusunga masiku anga a sabata.+ Chimenechi ndi chizindikiro pakati pa ine ndi inu mʼmibadwo yanu yonse, kuti mudziwe kuti ine Yehova ndakusankhani kukhala opatulika.
2 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale lopatulika kwa inu, likhale sabata la Yehova lopuma pa ntchito zanu zonse.+ Aliyense wogwira ntchito pa tsikuli adzaphedwa.+