-
Levitiko 26:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 ndipo mukadzakana malangizo anga,+ nʼkunyansidwa ndi zigamulo zanga mpaka kukana kutsatira malamulo anga onse, nʼkufika pophwanya pangano langa,+ 16 ine ndidzakuchitani zotsatirazi: Ndidzakulangani pokupangitsani kukhala ndi mantha, kudwala chifuwa chachikulu ndi kutentha kwa thupi koopsa, zimene zidzachititsa maso anu khungu ndi kukufooketsani. Simudzapindula ndi mbewu zimene mwafesa, chifukwa adani anu adzadya zokolola zanuzo.+
-