-
Yeremiya 49:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ponena za Edomu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Kodi nzeru zinatha ku Temani?+
Kodi anthu ozindikira sakuperekanso malangizo anzeru?
Kodi nzeru zawo zinawola?
8 Thawani! Bwererani!
Pitani kumalo otsika kuti mukakhale kumeneko, inu amene mukukhala ku Dedani!+
Chifukwa Esau ndidzamugwetsera tsoka
Nthawi yoti ndimupatse chilango ikadzafika.
-