4 Komanso kodi ndakulakwira chiyani
Iwe Turo ndi Sidoni ndiponso nonse amʼchigawo cha Filisitiya?
Kodi mukundichitira zimenezi pondibwezera zimene ndinachita?
Ngati mukundibwezera,
Ine ndidzakubwezerani mwamsanga ndiponso mofulumira zimene mwandichitirazo.+
5 Chifukwa chakuti mwatenga siliva ndi golide wanga,+
Ndipo mwabweretsa zinthu zanga zabwino kwambiri mu akachisi anu,
6 Komanso mwagulitsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kwa Agiriki,+
Kuti muwapititse kutali ndi dziko lawo,